Mateyu 18:5-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo amene adzalandira kamwana kamodzi kotereka cifukwa ca dzina langa, alandira Ine;

6. koma yense amene adzakhumudwitsa kamodzi ka tiana iti, takukhulupirira Ine, kumuyenera iye kuti mphero yaikuru ikolowekedwe m'khosi mwace, namizidwe poya pa nyanja.

7. Tsoka liri hdi dziko lapansi cifukwa ca zokhumudwitsa! pakuti sikutheka kuti zokhumudwitsa zileke kudza, koma tsoka liri ndi munthu amene cokhumudwitsaco cidza ndi iye.

8. Ndipo ngati dzanja lako, kapena phazi lako likukhumudwitsa iwe, ulidule, nulitaye; nkwabwino, kuti ulowe m'moyo wopunduka dzanja kapena phazi, koposa kuponyedwa m'moto wa nthawi zonse, uli ndi manja awiri kapena mapazi awiri.

9. Ndipo ngati diso lako likukhumudwitsa, ulikolowole, nulitaye: nkwabwino kuti ulowe m'moyo ndi diso limodzi koposa kuponyedwa m'gehena wamoto, uli ndi maso awiri.

10. Yang'anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang'ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo ao apenya cipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba. [

11. ]

12. Nanga muyesa bwanji? ngati munthu ali nazo nkhosa makumi khumi, ndipo ikasokera imodzi ya izo, kodi saleka zija makumi asanu ndi anai mphambu manu ndi zinai, napita kumapiri, kukafuna yosokerayo?

13. Ndimo akaipeza, indedi ndinena kwa inu, akondwera nayo koposa ndi makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi zinai zosasokera.

14. Comweco siciri cifuniro ca Atate wanu wa Kumwamba kuti mmodzi wa ang'ono awa atayike.

15. Ndipo ngati mbale wako akucimwira iwe, pita, numlangize pa nokha iwe ndi iye; ngati akumvera iwe, wambweza mbale wako.

16. Koma ngati samvera, onjeza kutenga ndi iwe wina mmodzi kapena awiri, kuti atsimikizidwe mau onse pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu.

17. Ndipo ngati iye samvera iwo, uuze Mpingo; ndipo ngati iye samveranso Mpingowo, akhale kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho.

18. Indetu ndinena kwa inu, Ziri zonse mukazimanga pa dziko lapansi zidzakhala zomangidwa Kumwamba: ndipo ziri zonse mukazimasula pa dziko lapansi, zidzakhala zomasulidwa Kumwamba.

19. Ndiponso ndinena kwa inu kuti ngati awiri ainu abvomerezana pansi pano cinthu ciri conse akacipempha, Atate wanga wa Kumwamba adzawacitira.

20. Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m'dzina langa, ndiri komweko pakati pao.

Mateyu 18