Mateyu 18:21-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Pamenepo Petro anadza, nati kwa Iye, Ambuye, mbale wanga adzandilakwira kangati, ndipo ine ndidzamkhululukira iye? kufikira kasanu ndi kawiri kodi?

22. Yesu ananena kwa iye, Sindinena kwa iwe kufikira kasanu ndi kawiri, koma kufikira makumi ananu ndi awiri kubwerezedwa kasanu ndi kawiri.

23. Cifukwa cace Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, mfumu, amene anafuna kuwerengera nao akapolo ace.

24. Ndipo pamene anayamba kuwerengera, anadza kwa iye ndi wina wamangawa wa ndalama za matalente zikwi khumi.

25. Koma popeza iye anasowa kanthu kombwezera, mbuye wace analamulira kuti iye agulitsidwe, ndi mkazi wace ndi ana ace omwe, ndi zonse ali nazo, kuti akabwezedwe mangawawo.

26. Cifukwa cace kapoloyo anagwadapansi, nampembedzera, nati, Mbuye, bakandiyembekezani ine, ndipo zonse ndidzazibwezera kwa inu.

27. Ndipo mbuye wa kapoloyo anagwidwa ndi cisoni mumtima, nammasula iye, namkhululukira ngongole.

28. Koma kapolo uyu, poturuka anapeza wina wa akapolo anzace yemwe anamkongola iye marupiya atheka makumi khumi, namgwira, namkanyanga pakhosi, nati, Bwezera cija unacikongola.

29. Pamenepo kapolo mnzaceyu anagwada pansi, nampempha iye, nati, Bakandiyembekeza ine, ndipo ndidzakubwezera.

30. Ndipo iye sanafuna; koma anamuka, namponya iye m'nyumba yandende, kufikira abwezere ngongole.

31. Cifukwa cace m'mene akapolo anzace anaona zocitidwazo, anagwidwa cisoni cacikuru, nadza, nalongosolera mbuye wao zonse zimene zinacitidwa.

32. Pomwepo mbuye wace anamuitana iye, nanena naye, Kapolo iwe weipa, ndinakukhululukira iwe mangawa onse aja momwe muja unandipempha ine;

33. kodi iwenso sukadamcitira kapolo mnzako cisoni, monga inenso ndinakucitira iwe cisoni?

34. Ndipo mbuye wace anakwiya, nampereka kwa azunzi, kufikira akambwezere iye mangawa onse.

Mateyu 18