10. ndipo anatumiza mnyamata, namdula mutu Yohane m'nyumba yandende.
11. Ndipo anautenga mutu wace m'mbizimo, naupatsa buthulo: ndipo iye anamuka nao kwa amace.
12. Ndipo ophunzira ace anadza, natola mtembo, nauika; ndipo anadza nauza Yesu.
13. Ndipo Yesu pakumva, anacokera kumeneko m'ngalawa, kunka ku malo acipululu pa yekha; ndipo makamu, pamene anamva, anamtsata Iye mumtunda kucokera m'midzi.
14. Ndipo Iye anaturuka, naona khamu lalikuru la anthu, nacitira iwo cifundo, naciritsa akudwala ao.
15. Ndipo pamene panali madzulo, ophunzira ace anafika kwa Iye, nanena, Malo ano nga cipululu, ndipo nthawi yapita tsopano; kauzeni makamuwo amuke, apite ku midzi kukadzigulira okha kamba.
16. Koma Yesu anati kwa iwo, Iwo alibe cifukwa ca kumukira, apatseni ndinu adye.
17. Koma iwo ananena kwa Iye, Ife tiribe kanthu pano koma mikate isanu, ndi nsomba ziwiri.
18. Ndipo Iye anati, Mudze nazo kuno kwa Ine.
19. Ndipo Iye analamulira makamu a anthu akhale pansi pamaudzu; ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo, ndipo m'mene anayang'ana kumwamba, anadalitsa, nanyema, napatsa mikateyo kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa makamuwo.
20. Ndipo anadya onse, nakhuta; ndipo anatola makombo otsala, mitanga khumi ndi iwiri yodzala.
21. Ndipo anadyawo anali amuna monga zikwi zisanu, kuwaleka akazi ndi ana.
22. Ndipo pomwepo Iye anafulumiza ophunzira alowe m'ngalawa, ndi kumtsogolera Iye ku tsidya lija, kufikira Iye atauza makamu amuke.
23. Ndipo pamene Iye anawauza makamuwo, anakwera m'phiri pa yekha, kukapemphera: ndipo pamene panali madzulo, Iye anakhala kumeneko yekha.
24. Koma pomwepo ngalawa idafika pakati pa nyanja, yozunzika ndi mafunde; pakuti mphepo inadza mokomana nao.