2. Ndipo makamu ambiri a anthu anasonkhanira kwa Iye, kotero kuti Iye analowa m'ngalawa, nakhala pansi, ndipo khamu lonse linaima pamtunda.
3. Ndipo Iye anawauzira zinthu zambiri m'mafanizo, nanena, Onani, wofesa anaturuka kukafesa mbeu,
4. Ndipo m'kufesa kwace zina zinagwa m'mbali mwa njira, ndipo zinadza mbalame, nizilusira izo.
5. Koma zina zinagwa pamiyala, pamene panalibe dothi lambiri; ndipo pomwepo zinamera, pakuti sizinakhala nalo dothi lakuya, Ndipo m'mene dzuwa linakwera zinapserera;
6. ndipo popeza zinalibe mizu zinafota.
7. Koma zina zinagwa paminga, ndipo mingayo inayanga, nizitsamwitsa izo.
8. Koma zina zinagwa pa nthaka yabwino, ndipo zinabala zipatso, zina za makumi khumi, zina za makumi asanu ndi limodzi, zina za makumi atatu.
9. Amene ali ndi makutu, amve.
10. Ndipo ophunzirawo anadza, nati kwa Iye, Cifukwa canji muphiphiritsira iwo m'mafanizo?
11. Ndipo Iye anayankha nati, Cifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziwa zinsinsi za Ufumu wa Kumwamba, koma sikunapatsidwa kwa iwo.
12. Pakuti yense amene ali nazo, kudzapatsidwa kwa iye, ndimo adzakhala nazo zocuruka; koma yense amene alibe, cingakhale comwe ali naco cidzacotsedwa kwa iye.
13. Cifukwa cace ndiphiphiritsira iwo m'mafanizo; cifukwa kuti akuona samaona, ndi akumva samamva, kapena samadziwitsa.
14. Ndipo adzacitidwa kwa iwo mau adanenera Yesaya, amene ati.Pakumva mudzamva, ndipo simudzazindikira konse;Pakupenya mudzapenya, ndipo simudzaona konse;
15. Cifukwa unalemera mtima wa anthuawa,Ndipo m'makutu ao anamva mogontha,Ndipo maso ao anatsinzina;Kuti asaone konse ndi maso,Asamve ndi makutu,Asazindikire ndi mtima wao,Asatembenuke,Ndipo ndisawaciritse iwo.
16. Koma maso anu ali odala, cifukwa apenya; ndi makutu anu cifukwa amva.