40. pakuti monga Yona anali m'mimba mwa cinsomba masiku atatu ndi usiku wace, comweco Mwana wa munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku wace.
41. 1 Anthu a ku Nineve adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; cifukwa 2 iwo anatembenuka mtima ndi kulalikira kwace kwa Yona; ndipo onani, wakuposa Y ona ali pano.
42. 3 Mfumu yaikazi ya kumwera adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; cifukwa iye anacokera ku mathero a dziko lapansi kudzamva nzeru ya Solomo; ndipo onani, wakuposa Solomo ali pano.
43. Koma mzimu wonyansa, utaturuka mwa munthu, umapitirira malo opanda madzi kufunafuna mpumulo, osaupeza.
44. Pomwepo unena, ndidzabwerera kunka kunyumba kwanga, konkuja ndinaturukako; ndipo pakufikako uipeza yopanda wokhalamo, yosesedwa ndi yokonzedwa.
45. Pomwepo upita, nutenga pamodzi ndi uwu mizimu yina inzace isanu ndi iwiri yoipa yoposa mwini yekhayo, ndipo ilowa, nikhalamo. Ndipo 4 matsirizidwe ace a munthu uyo akhala oipa oposa mayambidwe ace. Kotero kudzakhalanso kwa obadwa oipa amakono.
46. Pamene Iye anali cilankhulire ndi makamu, onani, amace ndi 5 abale ace anaima panja, nafuna kulankhula naye.
47. Ndipo munthu anati kwa Iye, Onani, amai wanu ndi abale anu aima pabwalo, nafuna kulankhula nanu.
48. Koma Iye anayankha, nati kwa iye wonenayo, Amai wanga ndani? ndi abale anga ndi ayani?
49. Ndipo anatambalitsa dzanja lace pa ophunzira ace, nati, Penyani amai wanga ndi abale anga!
50. Pakuti 6 ali yense amene adzacita cifuniro ca Atate wanga wa Kumwamba, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo wanga, ndi amai wanga.