13. Ndipo ngati nyumbayo iri yoyenera, mtendere wanu udze pa iyo, koma ngati siiri yoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu.
14. Ndipo yemwe sadzakulandirani inu, kapena kusamva mau anu, pamene mulikuturuka m'nyumbayo, kapena m'mudzimo, sansani pfumbi m'mapazi anu.
15. Indetu ndinena kwa inu, kuti, tsiku la kuweruza, mlandu wao wa Sodomu ndi Gomora udzacepa ndi wace wa mudzi umenewo.
16. Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa afisi; cifukwa cace khalani ocenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.
17. Koma cenjerani ndi anthu; pakuti adzakuperekani inu kwa akuru a mlandu, nadzakukwapulani inu m'masunagoge mwao;
18. Ndiponso adzamuka nanu kwa akazembe ndi mafumu cifukwa ca Ine, kukhala mboni ya kwa iwo, ndi kwa anthu akunja.
19. Koma pamene pali ponse angakuperekeni inu, musamadera nkhawa mudzalankhule bwanji kapena mudzanene ciani; pakuti cimene mudzacilankhula, cidzapatsidwa kwa inu nthawi yomweyo;
20. pakuti wolankhula si ndinu, koma Mzimu wa Atate wanu akulankhula mwa inu.
21. Ndipo mbale adzapereka mbale wace kuimfa, ndi atate mwana wace: ndipo ana adzatsutsa akuwabala, nadzawafetsa iwo.
22. Ndipo adzada inu anthu onse cifukwa ca dzina langa; koma iye wakupirira kufikira cimariziro, iyeyu adzapulumutsidwa.
23. Koma pamene angakuzunzeni inu m'mudzi uwu, thawirani mwina: indetu ndinena kwa inu, Simudzaitha mizinda ya Israyeli, kufikira Mwana wa munthu atadza.
24. Wophunzira saposa mphunzitsi wace, kapena kapolo saposa mbuye wace.
25. Kumkwanira wophunzira kuti akhale monga mphunzitsi wace, ndi kapolo monga mbuye. Ngati anamucha mwini banja Beelzebule, sadzaposa kodi kuwatero apabanja ace?
26. Cifukwa cace musaopa iwo; pakuti palibe kanthu kanabvundikiridwa, kamene sikadzaululidwa; kapena kanthu kobisika, kamene sikadzadziwika.
27. Cimene ndikuuzani inu mumdima, tacinenani poyera; ndi cimene mucimva m'khutu, mucilalikire pa macindwi nyumba.
28. Ndipo musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe m'gehena.