1. Ndipo pamene Iye anadziitanira ophunzira ace khumi ndi awiri, anapatsa iwo mphamvu pa mizimu yoipa, yakuiturutsa, ndi yakuciza nthenda iri yonse ndi zofoka zonse.
2. Ndipo maina ao a atumwiwo khumi ndi awiri ndi awa: woyamba Simoni wochedwa Petro, ndi Andreya mbale wace; Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi Yohane mbale wace;
3. Filipo, ndi Bartolomeyo; Tomasi, ndi Mateyu wamsonkhoyo; Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo;
4. Simoni Mkanani, ndi Yudasi Isikariote amenenso anampereka Iye.
5. Awa amene, khumi ndi awiriwa, Yesu anawatumiza, nawalangiza ndi kuti,Musapite ku njira ya kwa anthu akunja, ndi m'mudzi wa Asamariya musamalowamo:
6. koma makamaka mupite ku nkhosa zosokera za banja la Israyeli.
7. Ndipo pamene mulikupita lalikani kuti, Ufumu wa Kumwamba wayandikira.
8. Ciritsani akudwala, ukitsani akufa, konzani akhate, turutsani ziwanda: munalandira kwaulere, patsani kwaulere.
9. Musadzitengere ndalama zagolidi, kapena zasiliva, kapena zakobiri m'malamba mwanu;
10. kapena thumba la kamba la kunjira, kapena malaya awiri, kapena nsapato, kapena ndodo; pakuti wanchito ayenera kulandira zakudya zace.
11. Ndipo m'mzinda uliwonse, kapena m'mudzi mukalowamo, mufunsitse amene ali woyenera momwemo; ndipo bakhalani komweko kufikira muturukamo.
12. Ndipo polowa m'nyumba muwalankhule.
13. Ndipo ngati nyumbayo iri yoyenera, mtendere wanu udze pa iyo, koma ngati siiri yoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu.