22. Ndipo anadza ku Betsaida. Ndipo anadza naye kwa Iye munthu wakhungu, nampempha Iye kuti amkhudze.
23. Ndipo anamgwira dzanja munthu wakhunguyo, naturukira naye kunja kwa mudzi; ndipo atamthira malobvu m'maso mwace, naika manja pa iye, anamfunsa, Uona kanthu kodi?
24. Ndipo anakweza maso, nanena, Ndiona anthu; pakuti ndiwapenya ayendayenda ngati mitengo.
25. Pamenepo anaikanso manja m'maso mwace; ndipo anapenyetsa, naciritsidwa, naona zonse mbee.
26. Ndipo anamtumiza amuke kwao, nanena, Usalowe konse m'mudzi.
27. Ndipo anaturuka Yesu, ndi ophunzira ace, nalowa ku midzi ya ku Kaisareya wa Filipi; ndipo panjira anafunsa ophunzira ace, nanena nao, Kodi anthu anena kuti Ine ndine yani?
28. Ndipo ananena, nati, Yohane Mbatizi; ndi ena, Eliya; koma ena, Mmodzi wa aneneri.
29. Ndipo Iye anawafunsa, Koma inu munena kuti ndine yani? Petro anayankha nanena naye, Ndinu Kristu.