Genesis 2:6-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. kama inakwera nkhungu yoturuka pa dziko lapansi, niithirira ponse pamwamba pa nthaka.

7. Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m'mphuno mwace; munthuyo nakhala wamoyo.

8. Ndipo Yehova Mulungu anabzala m'munda ku Edene cakum'mawa; momwemo ndipo adaika munthu adamuumbayo.

9. Ndipo Yehova Mulungu anameretsa m'nthaka mitengo yonse yokoma m'maso ndi yabwino kudya; ndiponso mtengo wa moyo pakati pa mundapo, ndi mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa.

10. Ndipo unaturuka m'Edene mtsinje wakuthirira m'mundamo, m'menemo ndipo unalekana nucita miyendo inai.

11. Dzina la wakuyamba ndi Pisoni: umenewo ndiwo wozungulira dziko lonse la Havila, m'mene muli golidi;

12. golidi wa dziko ali wabwino; ndimonso muli bedola ndi mwala wasohamu.

Genesis 2