Ezekieli 40:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Caka ca makumi awiri ndi zisanu ca undende wathu, poyamba caka, tsiku lakhumi lamwezi, caka cakhumi ndi zinai atakantha mudziwo, tsiku lomwelo, dzanja la Mulungu linandikhalira; ndipo anamuka nane komweko.

2. M'masomphenya a Mulungu Iye anabwera nane m'dziko la Israyeli, nandikhalitsa pa phiri lalitali ndithu; pamenepo panali ngati mamangidwe a mudzi kumwela,

3. Ndipo anamuka nane komweko, ndipo taona, panali munthu, maonekedwe ace ngati amkuwa, ndi cingwe cabwazi m'dzanja lace, ndi bango loyesa nalo, naima kucipata iye.

4. Ndipo munthuyu anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, penya ndi maso ako, imva m'makutu mwako, nuike mtima wako pa zonse ndidzakuonetsa iwe; pakuti unatengedwa kudza kuno, kuti ndikuonetse izi; fotokozera nyumba ya Israyeli zonse uziona.

Ezekieli 40