Ezekieli 30:19-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Motero ndidzakwaniritsa maweruzo m'Aigupto, ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

20. Ndipo kunali caka cakhumi ndi cimodzi, mwezi woyamba, tsiku lacisanu ndi ciwiri la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,

21. Wabadwa ndi munthu iwe, ndatyola dzanja la Parao mfumu ya Aigupto, ndipo taona, silinamangidwa kuti lipole, kulikulunga ndi nsaru, kulilimbitsa ligwire lupanga.

22. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taona, Ine ndilimbana naye Parao mfumu ya Aigupto, ndidzatyola manja ace, lolimba ndi lotyokalo, ndi kutayitsa lupanga m'dzanja lace.

23. Ndipo ndidzamwaza Aaigupto mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa m'maiko.

24. Ndipo ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babulo, ndi kuika lupanga langa m'dzanja lace; koma ndidzatyola manja a Parao, ndipo adzabuula pamaso pace mabuulo a munthu wopyozedwa.

Ezekieli 30