8. Ndipo mwana wamkazi wa Farao ananena naye, Pita. Napita namwaliyo, nakaitana amace wa mwanayo.
9. Ndipo mwana wamkazi wa Farao ananena naye, Pita naye mwana uyu, ndi kundiyamwitsira iye, ndidzakupatsa mphotho yako. Ndipo mkaziyo anatenga mwanayo, namyamwitsa,
10. Ndipo atakula mwanayo, anapita naye kwa mwana wamkazi wa Farao, ndipo iye anakhala mwana wace. Ndipo anamucha dzina lace Mose, nati, Cifukwa ndinambvuula m'madzi.
11. Ndipo kunali masiku amenewo, atakula Mose, kuti anaturukira kukazonda abale ace, napenya akatundu ao; ndipo anaona munthu M-aigupto ali kukantha Mhebri, wa abale ace.
12. Ndipo anaunguza kwina ndi kwina, ndipo pamene anaona kuti palibe munthu, anakantha M-aigupto, namfotsera mumcenga.