Danieli 9:5-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. tacimwa, tacita mphulupulu, tacita zoipa, tapanduka, kupambuka ndi kusiya maneno anu ndi maweruzo anu;

6. sitinamvera atumiki anu aneneri, amene ananena m'dzina lanu kwa mafumu athu, akalonga athu, makolo athu, ndi anthu onse a m'dziko.

7. Ambuye, cilungamo nca Inu, koma kwa ife manyazi a nkhope yathu, monga lero lino; kwa anthu a Yuda, ndi kwa okhala m'Yerusalemu, ndi kwa Aisrayeli onse okhala pafupi ndi okhala kutali, ku maiko onse kumene mudawaingira, cifukwa ca kulakwa kwao anakulakwirani nako.

8. Ambuye, kwa ife kuli manyazi a nkhope yathu, kwa mafumu athu, kwa akalonga athu, ndi kwa makolo athu; pakuti takucimwirani.

9. Ambuye Mulungu wathu ndiye wacifundo, ndi wokhululukira; pakuti tampandukira Iye;

10. sitinamvera mau a Yehova Mulungu wathu, kuyenda m'malamulo ace anatiikirawo pamaso pathu, mwa atumiki ace aneneri.

Danieli 9