6. Ndipo wina anati kwa munthu wobvala bafuta, wokhala pamwamba pa madzi a mumtsinje, Cimariziro ca zodabwiza izi cidzafika liti?
7. Ndipo ndinamva munthuyo wobvala bafuta wokhala pamwamba pa madzi a mumtsinje, nakweza dzanja lace lamanja ndi lamanzere kumwamba, nalumbira pali Iye wokhala ndi moyo kosatha, kuti zidzacitika nthawi, ndi nthawi zina, ndi nusu; ndipo atatha kumwaza mphamvu ya anthu opatulikawo zidzatha izi zonse.
8. Ndinacimva ici, koma osacizindikira; pamenepo ndinati Mbuye wanga, citsiriziro ca izi nciani?
9. Ndipo anati, Pita Danieli; pakuti mauwo atsekedwa, nakomeredwa cizindikilo mpaka nthawi ya citsiriziro.
10. Ambiri adzadzitsuka ndi kudziyeretsa, nadzayesedwa ndi moto; koma oipa adzacita moipa; ndipo palibe mmodzi wa oipa adzazindikira; koma aphunzitsi ndiwo adzazindikira.
11. Ndipo kuyambira nthawi yoti idzacotsedwa nsembe yacikhalire, nicidzaimika conyansa cakupululutsa, adzakhalanso masiku cikwi cimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai.