7. Koma apo pophukira mizu yace adzauka wina m'malo mwace, ndiye adzafika kulimbana nalo khamu la nkhondo, nadzalowa m'linga la mfumu ya kumpoto, nadzacita molimbana nao, nadzawalaka;
8. ndi milungu yao yomwe, pamodzi ndi akalonga ao, ndi zipangizo zao zofunika za siliva ndi golidi adzazitenga kumka nazo ndende ku Aigupto; ndi zaka zace zidzaposa za mfumu ya kumpoto.
9. Ndipo adzalowa m'ufumu wa mfumu ya kumwela, koma adzabwera m'dziko lace lace.
10. Ndi ana ace adzacita nkhondo, nadzamemeza makamu a nkhondo akuru ocuruka, amene adzalowa, nadzasefukira, nadzapita; ndipo adzabwerera, nadzacita nkhondo mpaka linga lace.