Danieli 10:19-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Nati, Munthu wokondedwatu iwe, Usaope, mtendere ukhale nawe; limbika, etu limbika. Ndipo pamene ananena ndi ine ndinalimbikitsidwa, ndinati, Anene mbuye wanga; pakuti mwandilimbikitsa.

20. Pamenepo anati, Kodi udziwa cifukwa coti ndakudzera? ndipo tsopano ndibwerera kulimbana ndi kalonga wa Perisiya; ndipo pomuka ine, taonani, adzadza kalonga wa Helene.

21. Koma ndidzakufotokozera colembedwa pa lemba la coonadi; ndipo palibe wina wakudzilimbikitsa pamodzi ndi ine, kutsutsana ndi aja, koma Mikaeli kalonga wanu.

Danieli 10