5. Iye amene alakika adzambveka motero zobvala zoyera; ndipo sindidzafafaniza ndithu dzina lace m'buku la moyo, ndipo ndidzambvomereza dzina lace pamaso pa Atate wanga, ndi pamaso pa angelo ace.
6. Iye wakukhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo.
7. Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Filadelfeya lemba;Izi anena iye amene ali Woyera, iye amene ali Woona, iye wakukhala naco cifungulo ca Davide, iye wotsegula, ndipo palibe wina atseka; iye wotseka, ndipo palibe wina atsegula:
8. Ndidziwa nchito zako (taona, ndapatsa pamaso pako khomo lotseguka limene munthu sakhoza kutsekapo), kuti uli nayo mphamvu pang'ono, ndipo unasunga mau anga, osakana dzina langa.