2. Pakati pa khwalala lace, ndi tsidya ili la mtsinje, ndi tsidya lace lija panali mtengo wa moyo wakubala zipatso khumi ndi ziwiri, ndi kupatsa zipatso zace mwezi ndi mwezi; ndipo masamba a mtengo ndiwo akuciritsa nao amitundu.
3. Ndipo sipadzakhalanso temberero liri lonse; ndipo mpando wacifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa udzakhala momwemo; ndipo akapolo ace adzamtumikira iye,
4. nadzaona nkhope yace; ndipo dzina lace lidzakhala pamphumipao.
5. Ndipo sikudzakhalanso usiku; ndipo sasowa kuunika kwa nyali, ndi kuunika kwa dzuwa; cifukwa Ambuye Mulungu adzawaunikira; ndipo adzacita ufumu ku nthawi za nthawi.
6. Ndipo anati kwa ine, Mau awa ali okhulupirika ndi oona; ndipo Ambuye, Mulungu wa mizimu ya aneneri, anatuma mngelo wace kukaonetsera akapolo ace zimene ziyenera kucitika msanga.
7. Ndipo taonani, ndidza msanga. Wodala iye amene asunga mau a cinenero ca buku ili.
8. Ndipo ine Yohane ndine wakumva ndi wakupenya izi. Ndipo pamene ndinamva ndi kupenya, ndinagwa pansi kulambira pa mapazi a mngelo wakundionetsa izo.
9. Ndipo ananena kwa ine, Tapenya, usacite; ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako aneneri, ndi wa iwo akusunga mau a buku ili; lambira Mulungu.
10. Ndipo ananena ndi ine, Usasindikiza cizindikilo mau a cinenero ca buku ili; pakuti nthawi yayandikira.
11. Iye wakukhala wosalungama acitebe zosalungama; ndi munthu wonyansa akhalebe wonyansa; ndi iye wakukhala wolungama acitebe colungama; ndi iye amene ali woyera akhalebe woyeretsedwa.
12. Taonani, ndidza msanga; ndipo mphotho yanga ndiri nayo yakupatsa yense monga mwa nchito yace.