Cibvumbulutso 11:11-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo atapita masiku atatu ndi nusu lace mzimu wamoyo wocokera kwa Mulungu unawalowera, ndipo anakhala ciriri; ndipomantha akuru anawagwera iwo akuwapenya.

12. Ndipo anamva mau akuru akucokera Kumwamba akunena nao, Kwerani kuno. Ndipo anakwera kumka Kumwamba mumtambo; ndipo adani ao anawapenya.

13. Ndipo panthawipo panali cibvomezi cacikuru, ndipo limodzi la magawo khumi a mudzi Iidagwa; ndipo anaphedwa m'cibvomezico anthu zikwi zisanu ndi ziwiri; ndipo otsalawo anakhala amantha, napatsa ulemerero kwa Mulungu wa m'Mwamba.

Cibvumbulutso 11