2 Samueli 10:12-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ulimbike mtima, ndipo ticite camuna lero cifukwa ca anthu athu ndi midzi ya Mulungu wathu; Yehova nacite comkomera.

13. Comweco Yoabu ndi anthu amene anali naye anayandikira kuponyana nkhondo ndi Aaramu. Ndipo iwowa anathawa pamaso pace.

14. Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti Aaramu anathawa, iwonso anathawa pamaso pa Abisai, nalowa m'mudzimo. Ndipo Yoabu anabwera kucokera kwa ana a Amoni, nafika ku Yerusalemu.

15. Ndipo pamene Aaramu anaona kuti Aisrayeli anawathyola, anasonkhana pamodzi.

16. Ndipo Hadarezeri anatumiza mthenga nakatenga Aaramu a ku tsidya la cimtsinje; iwo nafika ku Helamu, ndi Sobaki kazembe wa khamu la nkhondo la Hadarezeri anawatsogolera.

2 Samueli 10