20. Ndipo zikho zomwera zonse za Solomo zinali zagolidi, ndi zipangizo zonse za nyumba yochedwa Nkhalango ya Lebano zinali za golidi woona; siliva sanayesedwa kanthu m'masiku a Solomo.
21. Pakuti zombo za mfumu zinayenda ku Tarisi ndi anyamata a Huramu; zombo za ku Tarisi zinadza kamodzi zitapita zaka zitatu, ndi kubwera nazo golidi, ndi siliva, minyanga, ndi apusi, ndi mbalame za zitsukwa zazitali za mawanga mawanga.
22. Mamwemo mfumu Solomo inaposa mafumu onse a pa dziko lapansi, kunena za cuma ndi nzeru.
23. Ndipo mafumu onse a pa dziko lapansi anafuna nkhope ya Solomo, kudzamva nzeru zace Mulungu adazilonga m'mtima mwace.
24. Nabwera nao munthu yense mtulo wace, zipangizo zasiliva, ndi zipangizo zagolidi, zobvala, ndi zobvala za nkhondo, ndi zonunkhira, akavalo, ndi nyuru; momwemo caka ndi caka.
25. Ndipo Solomo anali nazo zipinda zikwi zinai za akavalo ndi magareta, ndi apakavalo zikwi khumi ndi ziwiri; nawaika m'toidzi ya magareta, ndi m'Yerusalemu kwa mfumu.
26. Ndipo analamulira mafumu onse kuyambira ku Firate kufikira ku dziko la Afilisti, ndi ku malire a ku Aigupto.
27. Ndipo mfumu inacurukitsa siliva m'Yerusalemu ngati miyala; ndi mikungudza anailinganiza ndi mikuyu iri kumadambo kucuruka kwace.
28. Ndipo anakamtengera Solomo akavalo ku Aigupto, ndi ku maiko onse.
29. Macitidwe ena tsono a Solomo, oyamba ndi otsiriza, salembedwa kodi m'buku la mau a Natani mneneri ndi m'zonenera za Ahiya wa ku Silo, ndi m'masomphenya a Ido mlauli za Yerobiamu mwana wa Nebati?