18. pamenepo ndidzakhazikitsa mpando wacifumu wa ufumu wako, monga ndinapangana ndi Davide atate wako, ndi kuti, Sadzakusowa munthu wokhala mfumu m'Israyeli.
19. Koma mukabwerera inu, ndi kusiya malemba anga, ndi malamulo anga, amene ndaika pamaso panu, ndi kumuka ndi kutumikira milungu yina ndi kuilambira;
20. pamenepo ndidzawazula m'dziko langa limene ndinawapatsa; ndi nyumba yino ndinaipatulira dzina langa ndidzaitaya, osaionanso, ndi kuiyesa mwambi ndi mnyozo mwa mitundu yonse ya anthu.
21. Ndi munthu yense wakupita pa nyumba iyi yaitali adzadabwa nayo, nadzati, Yeliova ana tero ndi dziko lino ndi nyumba yino cifukwa ninji?
22. Ndipo adzayankha, Popeza anasiya Yehova Mulungu wa makolo ao amene anawaturutsa m'dziko la Aigupto, nagwira milungu yina, nailambira ndi kuitumikira; cifukwa cace anawagwetsera coipa ici conse.