3. Ndipo msonkhano wonse unapangana pangano ndi mfumu m'nyumba ya Mulungu. Ndipo ananena nao, Taonani, mwana wa mfumu adzakhala mfumu monga Yehova ananena za ana a Davide.
4. Cimene muzicita ndi ici: limodzi la magawo atatu mwa inu olowera dzuwa la Sabata, la ansembe ndi Alevi, akhale olindirira pakhomo;
5. ndi limodzi la magawo atatu likhale ku nyumba ya mfumu; ndi limodzi la magawo atatu ku cipata ca maziko; ndi anthu onse akhale m'mabwalo a nyumba ya Yehova.
6. Koma asalowe mmodzi m'nyumba ya Yehova, ansembe okha, ndi Alevi otumikira, alowe iwowa; pakuti ndiwo opatulika; koma anthu onse asunge udikiro wa Yehova.
7. Ndipo Alevi amzinge mfumu pozungulirapo, yense ndi zida zace m'dzanja mwace; ndipo ali yense wolowa m'nyumba aphedwe; nimukhale inu pamodzi ndi mfumu pakulowa ndi pakuturuka iye.
8. Momwemo Alevi ndi Ayuda onse anacita monga mwa zonse anawauza Yehoyada wansembe; natenga yense amuna ace alowe dzuwa la Sabata pamodzi ndi oturuka dzuwa la Sabata; pakuti Yehoyada wansembe sanamasula zigawo.