2 Mbiri 13:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo caka cakhumi mphambu zisanu ndi zitatu ca Yerobiamu, Abiya analowa ufumu wa Yuda.

2. Anakhala mfumu m'Yerusalemu zaka zitatu; ndi dzina la mace ndiye Mikaya mwana wamkazi wa Uriyeli wa ku Gibeya. Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobiamu.

3. Ndipo Abiya anayambana nkhondo ali ndi khamu la ngwazi za nkhondo, amuna osankhika zikwi mazana anai; Yerobiamu atandandalitsa nkhondo yace ilimbane naye ndi amuna osankhika zikwi mazana asanu ndi atatu, ndiwo ngwazi zamphamvu.

4. Ndipo Abiya anaimirira pa phiri la Zemaraimu, ndilo ku mapiri a Efraimu, nati, Mundimvere Yerobiamu ndi Aisrayeli onse;

5. simudziwa kodi kuti Yehova Mulungu wa Israyeli anapereka ciperekere ufumu wa Israyeli kwa Davide, kwa iye ndi ana ace, ndi pangano la mcere?

6. Koma Yerobiamu mwana wa Nebati mnyamata wa Solomo mwana wa Davide anauka, napandukana ndi mbuye wace.

7. Ndipo anamsonkhanira amuna acabe, anthu opanda pace, ndiwo anadzilimbikitsa kutsutsana naye Rehabiamu mwana wa Solomo, muja Rehabiamu anali mnyamata ndi woolowa mtima, wosakhoza kuwalaka.

8. Ndipo tsopano, mukuti mudzilimbikitse kutsutsana nao ufumu wa Yehova m'dzanja la ana a Davide; ndinu aunyinji ambiri, ndi pamodzi nanu ana a ng'ombe agolidi adawapanga Yerobiamu akhale milungu yanu.

9. Simunapitikitsa kodi ansembe a Yehova, ana a Aroni, ndi Alevi, ndi kudziikira ansembe monga amacita anthu a m'maiko ena? kuti ali yense wakudza kudzipatulira ndi mwana wa ng'ombe, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, yemweyo ndiye wansembe wa iyo yosati milungu.

2 Mbiri 13