2 Mbiri 1:3-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo Solomo ndi khamu lonse pamodzi naye anamuka ku msanje wa ku Gibeoni; pakuti kumeneko kunali cihema cokomanako ca Mulungu adacimanga Mose mtumiki wa Yehova m'cipululu.

4. Koma likasa la Mulungu Davide adakwera nalo kucokera ku Kiriyati Yearimu kumka kumene Davide adalikonzeratu malo; pakuti adaliutsiratu hema ku Yerusalemu.

5. Guwa la nsembe lomwe lamkuwa, adalipanga Bezaleli mwana wa Uri mwana wa Huri linali komweko, ku khomo la kacisi wa Yehova; ndipo Solomo ndi khamulo anafunako.

6. Nakwerako Solomo ku guwa la nsembe pamaso pa Yehova linali ku cihema cokomanako, napereka pamenepo nsembe zopsereza cikwi cimodzi.

7. Usiku womwewo Mulungu anaonekera kwa Solomo, nati kwa iye, Pempha comwe ndikupatse.

2 Mbiri 1