2. Iye anali ndi mwana wamwamuna dzina lace Sauli, mnyamata wokongola; pakati pa anthu onse a Israyeli panalibe wina wokongola ngati iye; anali wamtali, anthu onse ena anamlekeza m'cifuwa.
3. Ndipo aburu a Kisi, atate wa Sauli, analowerera. Ndipo Kisi anati kwa Sauli mwana wace, Utenge mnyamata mmodzi, nunyamuke, kukafuna aburuwo.
4. Ndipo anapyola dziko lamapiri la Efraimu, napyola dziko la Salisa, koma sanawapeza; pamenepo anapyolanso dziko la Salimu; koma panalibe pamenepo, napyola dziko la Abenjamini, osawapeza.
5. Pamene anafika ku dziko la Zufi, Sauli anamuuza mnyamata amene anali naye, kuti, Tiye tibwerere; kuti atate wanga angaleke kusamalira aburuwo, ndi kutenga nkhawa cifukwa ca ife.
6. Koma ananena naye, Onatu, m'mudzi muno muli munthu wa Mulungu, ndiye munthu anthu amcitira ulemu; zonse azinena zicitika ndithu; tiyeni tipite komweko, kapena adzakhoza kutidziwitsa zimene tirikuyendera.