52. Merayoti mwana wace, Amariya mwana wace, Ahitubu mwana wace,
53. Zadoki mwana wace, Ahimaazi mwana wace.
54. Pokhala pao tsono monga mwa madera ao m'malire mwao ndi awa: kwa ana a Aroni a mabanja a Akobati, pakuti maere oyamba adagwera iwowa,
55. kwa iwo anapereka Hebroni m'dziko la Yuda, ndi podyetsa pace pozungulira pace;
56. koma minda ya mudzi ndi miraga yace anapatsa Kalebi mwana wa Yefune.
57. Ndi kwa ana a Aroni anapereka midzi yopulumukirako: Hebroni, ndi Libina ndi mabusa ace, ndi Yatiri, ndi Esitemowa ndi mabusa ace,
58. ndi Hileni ndi mabusa ace, ndi Debiri ndi mabusa ace,
59. ndi Asani ndi mabusa ace, ndi Betesemesi ndi mabusa ace;
60. ndi ku pfuko la Benjamini Geba ndi mabusa ace, ndi Alemeti ndi mabusa ace, ndi Anatoti ndi mabusa ace. Midzi yao yonse mwa mabanja ao ndiyo midzi khumi ndi itatu.
61. Ndipo otsala a ana a Kohati analandira mwa maere, motapa pa mabanja a pfuko, pa pfuko la Manase logawika pakati, midzi khumi.
62. Ndi kwa ana a Gerisomu monga mwa mabanja ao, motapa pa pfuko la Isakara, ndi pa pfuko la Aseri, ndi pa pfuko la Nafitali, ndi pa pfuko la Manase m'Basana, midzi khumi ndi itatu.
63. Ana a Merari analandira mwa maere monga mwa mabanja ao, motapa pa pfuko la Rubeni, ndi pa pfuko la Gadi, ndi pa pfuko la Zebuluni, midzi khumi ndi iwiri.
64. Ndipo ana a Israyeli anapatsa Alevi midzi ndi mabusa ao.
65. Ndipo anapatsa mwamaere, motapa pa pfuko la ana a Yuda, ndi pa pfuko la Simeoni, ndi pa pfuko la ana a Benjamini, midzi iyi yochulidwa maina ao.
66. Ndi mabanja ena a ana a Kohati anali nayo midzi ya malire ao, yotapa pa pfuko la Efraimu.
67. Ndipo anawapatsa midzi yopulumukiramo: Sekemu ndi mabusa ace ku mapiri a Efraimu, Gezeri ndi mabusa ace,
68. ndi Yokimeamu ndi mabusa ace, ndi Betihoroni ndi mabusa ace,