1 Mbiri 23:1-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Atakalamba tsono Davide ndi kucuruka masiku, iye analonga mwana wace Solomo akhale mfumu ya Israyeli.

2. Ndipo anasonkhanitsa akuru onse a Israyeli, ndi ansembe ndi Alevi.

3. Ndipo anawerengedwa Alevi oyambira zaka makumi atatu ndi mphambu, ndipo ciwerengo cao kuwawerenga mmodzi mmodzi ndico amuna zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu.

4. A iwowa zikwi makumi awiri mphambu zinai anayang'anira nchito ya nyumba ya Yehova, ndi zikwi zisanu ndi cimodzi ndiwo akapitao ndi oweruza,

5. ndi zikwi zinai odikira; ndi zikwi zinai analemekeza Yehova ndi zoyimbira zimene ndinazipanga, anati Davide, kuti alemekeze nazo.

6. Ndipo Davide anawagawa magawo monga mwa ana a Levi: Gerisomu, Kohati, ndi Merari.

7. A Agerisomu: Ladani ndi Simeyi,

8. Ana a Ladani: wamkuru ndi Yehieli, ndi Zethamu, ndi Yoeli; atatu.

9. Ana a Simeyi: Selomoti, ndi Hazieli, ndi Hanani; atatu. Ndiwo akuru a nyumba za makolo a Ladani.

10. Ndi ana a Simeyi: Yahati, Zina, ndi Yeusi, ndi Beriya. Awa anai ndiwo ana a Simeyi.

11. Wamkuru wa iwo ndi Yahati, mnzace ndi Ziza; koma Yeusi ndi Beriya analibe ana ambiri, potero anakhala nyumba ya kholo yowerengedwa pamodzi.

12. Ana a Kohati: Amiramu, Izara, Hebroni, ndi Uzieli; anai.

13. Ana a Amiramu: Aroni, ndi Mose; ndipo Aroni anasankhidwa kuti apatule zopatulikitsa, iye ndi ana ace, kosalekeza, kufukiza pamaso pa Yehova, kumtumikira, ndi kudalitsa m'dzina lace kosatha.

14. Kunena za Mose munthu wa Mulunguyo, ana ace anaehulidwa mwa pfuko la Levi.

15. Ana a Mose: Gerisomu, ndi Eliezeri.

16. Ana a Gerisomu: wamkuru ndi Sebuyeli.

17. Ndi ana a Eliezeri: wamkuru ndi Rehabiya. Ndipo Eliezeri analibe ana ena, koma ana a Rehabiya anacuruka kwambiri.

18. Ana a Izara: wamkuru ndiye Selomiti.

1 Mbiri 23