Ana a Amiramu: Aroni, ndi Mose; ndipo Aroni anasankhidwa kuti apatule zopatulikitsa, iye ndi ana ace, kosalekeza, kufukiza pamaso pa Yehova, kumtumikira, ndi kudalitsa m'dzina lace kosatha.