1. Atakalamba tsono Davide ndi kucuruka masiku, iye analonga mwana wace Solomo akhale mfumu ya Israyeli.
2. Ndipo anasonkhanitsa akuru onse a Israyeli, ndi ansembe ndi Alevi.
3. Ndipo anawerengedwa Alevi oyambira zaka makumi atatu ndi mphambu, ndipo ciwerengo cao kuwawerenga mmodzi mmodzi ndico amuna zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu.
4. A iwowa zikwi makumi awiri mphambu zinai anayang'anira nchito ya nyumba ya Yehova, ndi zikwi zisanu ndi cimodzi ndiwo akapitao ndi oweruza,
5. ndi zikwi zinai odikira; ndi zikwi zinai analemekeza Yehova ndi zoyimbira zimene ndinazipanga, anati Davide, kuti alemekeze nazo.
6. Ndipo Davide anawagawa magawo monga mwa ana a Levi: Gerisomu, Kohati, ndi Merari.
7. A Agerisomu: Ladani ndi Simeyi,
8. Ana a Ladani: wamkuru ndi Yehieli, ndi Zethamu, ndi Yoeli; atatu.
9. Ana a Simeyi: Selomoti, ndi Hazieli, ndi Hanani; atatu. Ndiwo akuru a nyumba za makolo a Ladani.
10. Ndi ana a Simeyi: Yahati, Zina, ndi Yeusi, ndi Beriya. Awa anai ndiwo ana a Simeyi.
11. Wamkuru wa iwo ndi Yahati, mnzace ndi Ziza; koma Yeusi ndi Beriya analibe ana ambiri, potero anakhala nyumba ya kholo yowerengedwa pamodzi.
12. Ana a Kohati: Amiramu, Izara, Hebroni, ndi Uzieli; anai.
13. Ana a Amiramu: Aroni, ndi Mose; ndipo Aroni anasankhidwa kuti apatule zopatulikitsa, iye ndi ana ace, kosalekeza, kufukiza pamaso pa Yehova, kumtumikira, ndi kudalitsa m'dzina lace kosatha.