1 Mbiri 17:3-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo usiku womwewo mau a Mulungu anadzera Natani, ndi kuti,

4. Kauze Davide mtumiki wanga, Atero Yehova, Usandimangire nyumba yokhalamo;

5. pakuti sindinakhala m'nyumba kuyambira tsiku tija ndinakwera naye Israyeli, kufikira lero Gno; koma wa m'hema m'hema Ine, ndi wa m'kacisi m'kacisi,

6. Pali ponse ndinayenda nao Aisrayeli onse ndinanena kodi mau ndi woweruza ali yense wa Israyeli, amene ndinamuuza adyetse anthu anga, ndi kuti, Mwalekeranji kundimangira nyumba yamikungudza?

7. Cifukwa cace tsono, uzitero naye mtumiki wanga Davide, Atero Ambuye wa makamu, Ndinakutenga kubusa potsata iwe nkhosa, kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Israyeli;

8. ndipo ndakhala ndi iwe kuli konse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndakubukitsira dzina lakunga dzina la akuru okhala padziko.

9. Ndipo ndaikira anthu anga Israyeli malo, ndi kuwaoka, kuti akhale m'malo mwao osasunthikanso; ndi ana osalungama sadzawapululanso monga poyamba paja;

10. ndi kuyambira kuja ndinaika oweruza ayang'anire anthu anga Israyeli; ndipo ndagonjetsa adani ako onse. Ndikuuzanso kuti Yehova adzakumangira banja.

11. Ndipo kudzacitika, atakwanira masiku ako kuti uzipita kukhala ndi makolo ako, ndidzaukitsa mbeu yako pambuyo pako, ndiye wa ana ako; ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wace.

12. Iye adzandimangira nyumba; ndipo ndidzakhazikitsa mpando wacifumu wace kosatha.

13. Ndidzakhala atate wace, ndi iye adzakhala mwana wanga; ndipo sindidzamcotsera cifundo canga monga muja ndinacotsera iye amene anakhala usanakhale iwe;

1 Mbiri 17