1 Mbiri 17:12-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Iye adzandimangira nyumba; ndipo ndidzakhazikitsa mpando wacifumu wace kosatha.

13. Ndidzakhala atate wace, ndi iye adzakhala mwana wanga; ndipo sindidzamcotsera cifundo canga monga muja ndinacotsera iye amene anakhala usanakhale iwe;

14. koma ndidzamkhazikitsa m'nyumba mwanga, ndi m'ufumu wanga kosatha; ndi mpando wa cifumu wace udzakhazikika kosatha.

15. Monga mwa mau awa onse, ndi monga mwa masomphenya awa onse, momwemo Natani analankhula ndi Davide.

16. Pamenepo mfumu Davide analowa nakhala pamaso pa Yehova, nati, Ndine yani, Yehova Mulungu, ndi nyumba yanga njotani kuti mwandifikitsa mpaka pano?

17. Ndipo ici ncacing'ono pamaso panu, Mulungu, koma mwanena za nyumba ya mtumiki wanu nthawi yam'tsogolo ndithu, ndipo mwandiyesera ngati munthu womveka, Yehova Mulungu.

18. Anenenjinso Davide kwa Inu za ulemu wocitikira mtumiki wanu? pakuti mudziwa mtumiki wanu.

19. Yehova, cifukwa ca mtumiki wanu, ndi monga mwa mtima wanu, mwacita ukulu uwu wonse, kundidziwitsa zazikuru izi zonse.

20. Yehova, palibe wina wonga inu, palibenso Mulungu wina koma Inu; monga mwa zonse tazimva m'makutu mwathu.

21. Ndiwo ayani akunga anthu anu Israyeli, mtundu wa pa wokha wa pa dziko lapansi, amene Mulungu anakadziombolera mtundu wa anthu, kudzibukitsira dzina, mwa zazikuru ndi zoopsa, pakupitikitsa amitundu pamaso pa anthu anu amene munawaombola m'Aigupto?

22. Pakuti anthu anu Israyeli mudawayesa anthu anu anu kosatha; ndipo Inu, Yehova, munayamba kukhala Mulungu wao.

23. Ndipo tsopano, Yehova, akhazikike kosalekeza mau mudanenawa za mtumiki wanu, ndi za nyumba yace, nimucite monga mwanena.

24. Inde likhazikike dzina lanu, likulitsidwe kosalekeza, ndi kuti, Yehova wa makamu ndiye Mulungu wa Israyeli; akhalira Israyeli Mulungu; ndi nyumba ya Davide mtumiki wanu ikhazikika pamaso panu.

25. Pakuti Inu, Mulungu wanga, mwaululira mtumiki wanu kuti mudzammangira banja; momwemo mtumiki wanu waona mtima wakupemphera pamaso panu.

1 Mbiri 17