30. Njenjemerani pamaso pace, inu dziko lonse lapansi,Dziko lokhalamo anthu lomwe lakhazikika, kuti silingagwedezeke.
31. Kukondwerere kumwamba, ndi dziko lapansi lisekerere;Anene mwa amitundu, Yehova acita ufumu.
32. Nyanja ikukume m'kudzala kwace,Munda ukondwerere, ndi zonse ziri m'mwemo;
33. Pamenepo mitengo yonse ya kunkhalango idzapfuula mokondwera pamaso pa Yehova;Pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi,
34. Yamikani Yehova; pakuti iye ndiye wabwino;Pakuti cifundo cace ncosatha.
35. Nimunene, Tipulumutseni, Mulungu wa cipulumutso cathu;Mutisokolotse ndi kutilanditsa kwa amitundu,Kuti tiyamike dzina lanu loyera,Ndi kudzitamandira naco cilemekezo canu.
36. Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israyeli,Kuyambira kosayamba kufikira kosatha.Ndipo anthu onse anati, Amen! nalemekeza Yehova.
37. Ndipo anasiyako ku likasa la cipangano la Yehova Asafu ndi abale ace, atumikire kulikasa kosalekeza, monga umo mudzafunika tsiku ndi tsiku;
38. ndi Obedi Edomu, ndi abale ace makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu ndi atatu; ndi Obedi Edomu mwana wa Yedutuni ndi Hosa akhale odikira;
39. ndi Zadoki wansembe, ndi abale ace ansembe, ku kacisi wa Yehova, pa msanje unali ku Gibeoni;
40. kupereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa guwa la nsembe zopsereza, kosalekeza, m'mawa ndi madzulo, monga mwa zonse zilembedwa m'cilamulo ca Yehova adacilamulira Israyeli;
41. ndi pamodzi nao Hemani, ndi Yedutuni, ndi osankhika otsalawo, ochulidwa maina, kuyamika Yehova; pakuti cifundo cace ncosatha;
42. ndi pamodzi nao Hemani, ndi Yedutuni, ndi malipenga ndi nsanje za iwo akumveketsadi, ndi zoyimbira nyimbo za Mulungu; ndi ana a Yedutuni anakhala kucipata.
43. Ndipo anacoka anthu onse, yense ku nyumba yace, nabwera Davide kudalitsa nyumba yace.