1 Mbiri 16:22-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndi kuti, Musamakhudza odzozedwa anga,Musamacitira coipa aneneri anga,

23. Myimbireni Yehova, inu dziko lonse lapansi,Lalikirani cipulumutso cace tsiku ndi tsiku,

24. Fotokozerani ulemerero wace mwa amitundu,Zodabwiza zace mwa mitundu yonse ya anthu.

25. Pakuti Yehova ali wamkuru, nayenera kulemekezedwa kwakukulu;Ayenera amuope koposa milungu yonse.

26. Pakuti milungu ya mitundu ya anthu ndiyo mafano;Koma Yehova analenga zakumwamba.

27. Pamaso pace pali ulemu ndi ukulu,M'malo mwace muli mphamvu ndi cimwemwe.

28. Mcitireni Yehova, inu mafuko a mitundu ya anthu,Mcitireni Yehova ulemerero ndi mphamvu.

29. Mcitireni Yehova ulemerero wa dzina lace;Bwerani naco copereka, ndipo fikani pamaso pace;Lambirani Yehova m'ciyero cokometsetsa,

30. Njenjemerani pamaso pace, inu dziko lonse lapansi,Dziko lokhalamo anthu lomwe lakhazikika, kuti silingagwedezeke.

31. Kukondwerere kumwamba, ndi dziko lapansi lisekerere;Anene mwa amitundu, Yehova acita ufumu.

32. Nyanja ikukume m'kudzala kwace,Munda ukondwerere, ndi zonse ziri m'mwemo;

33. Pamenepo mitengo yonse ya kunkhalango idzapfuula mokondwera pamaso pa Yehova;Pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi,

34. Yamikani Yehova; pakuti iye ndiye wabwino;Pakuti cifundo cace ncosatha.

35. Nimunene, Tipulumutseni, Mulungu wa cipulumutso cathu;Mutisokolotse ndi kutilanditsa kwa amitundu,Kuti tiyamike dzina lanu loyera,Ndi kudzitamandira naco cilemekezo canu.

1 Mbiri 16