2. Ndipo Davide anazindikira kuti Yehova adamkhazikitsa mfumu ya Israyeli; pakuti ufumu wace unakwezekadi, cifukwa ca anthu ace Israyeli.
3. Ndipo Davide anatenga akazi ena ku Yerusalemu, nabala Davide ana amuna ndi akazi ena.
4. Maina a ana anali nao m'Yerusalemu ndi awa: Samna, ndi Sobabu Natani, ndi Solomo,
5. ndi Ibara, ndi Elisua, ndi Elipeleti,
6. ndi Noga, ndi Nefegi, ndi Yafiya,
7. ndi Elisama, ndi Beliyada, ndi Elifeleti.
8. Pamene Afilisti anamva kuti anamdzoza Davide akhale mfumu ya Aisrayeli onse, Afilisti onse anakwera kufunafuna Davide; ndipo Davide anamva, nawaturukira.
9. Afilisti tsono anafika, nafalikira m'cigwa ca Refaimu.