1 Mbiri 12:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Anadzawo kwa Davide ku Zikilaga, akali citsekedwere cifukwa ca Sauli mwana wa Kisi, ndi awa; ndiwo mwa amphamvuwo omthandiza kunkhondo.

2. Anakoka mauta; naponya miyala, naponya mibvi ndi uta ndi dzanja lamanja ndi lamanzere lomwe; ndiwo a abale ace a Sauli, Abenjamini.

3. Mkuru wao ndiye Ahiezeri, ndi Yoasi, ana a Semaa wa ku Gibeya; ndi Yezieli, ndi Peleti, ana a Azmaveti; ndi Beraka, ndi Yehu wa ku Anatoti,

4. ndi Ismaya wa ku Gibeoni, wamphamvu mwa makumi atatuwo ndi woyang'anira makumi atatuwo, ndi Yeremiya, ndi Yahazieli, ndi Yohanani, ndi Yozabadi wa ku Gedera,

5. Eluzai, ndi Yerimoti, ndi Bealiya, ndi Semariya, ndi Sefatiya wa ku Harupi,

6. Elikana, ndi Isiya, ndi Azereli, ndi Yoezeri, ndi Yasobeamu ndiwo Akora;

1 Mbiri 12