1 Mbiri 11:21-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Mwa atatuwa iye anali waulemu woposa awiriwa, nasanduka mkuru wao; koma sanafikana nao atatu oyamba aja.

22. Benaya mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi ya ku Kabzeeli, wocita zazikuru, anapha ana awiri a Ariyeli wa ku Moabu; anatsikanso, napha mkango m'kati mwa dzenje nyengo ya cipale cofewa.

23. Anaphanso M-aigupto munthu wamkuru, msinkhu wace mikono isanu, ndi m'dzanja la M-aigupto munali mkondo ngati mtanda woombera nsaru; ndipo anamtsikira ndi ndodo, nakwatula mkondo m'dzanja la M-aigupto, namupha ndi mkondo wace womwe.

24. Izi anazicita Benaya mwana wa Yehoyada, namveka dzina mwa atatu amphamvuwo.

25. Taonani, anali wa ulemu woposa makumi atatuwo, koma sanafikana atatu oyamba aja; ndipo Davide anamuika mkuru wa olindirira ace.

26. Ndipo amphamvuwo a magulu a nkhondo ndiwo Asaheli mbale wa Yoabu, Elanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu,

27. Samoti Mharori, Helezi Mpeloni,

28. Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekoi, Abiezeri wa ku Anatoti,

1 Mbiri 11