1. Ndipo Benihadadi mfumu ya Aramu anamemeza khamu lace lonse la nkhondo; ndi mafumu makumi atatu mphambu awiri anali naye, pamodzi ndi akavalo ndi magareta; nakamangira Samaria misasa, naponyana nao nkhondo.
2. Natumiza mithenga lrumudzi kwa Ahabu mfumu ya Israyeli, nati kwa iye,
3. Atero Benihadadi, Siliva wako ndi golidi wako ndi wanga, akazi ako ndi ana ako omwe okometsetsawo ndi anga.