Zekariya 8:4-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Atero Yehova wa makamu: M'miseu ya Yerusalemu mudzakhalanso amuna ndi akazi okalamba, yense ndi ndodo yace m'dzanja lace cifukwa ca ukalamba wace.

5. Ndi m'miseu ya mudzi mudzakhala ana amuna ndi akazi akusewera m'miseu yace.

6. Atero Yehova wa makamu: Cikakhala codabwitsa pamaso pa otsala a anthu awa masiku awo, kodi cidzakhalanso codabwitsa pamaso panga? ati Yehova wa makamu.

7. Atero Yehova wa makamu: Taonani, ndidzapulumutsa anthu anga m'dziko la kum'mawa, ndi m'dziko la kumadzulo;

8. ndipo ndidzabwera nao, nadzakhala m'kati mwa Yerusalemu; ndipo iwo adzakhala anthu anga, nanenso ndidzakhala Mulungu wao, m'coonadi ndi m'cilungamo.

9. Atero Yehova wa makamu: Alimbike manja anu, inu akumva masiku ano mau awa pakamwa pa aneneri amene anakhalako tsiku lakuikidwa maziko a nyumba ya Yehova wa makamu, ndiyo Kacisi, kuti amangidwe.

Zekariya 8