Zefaniya 1:13-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo zolemera zao zidzakhala zakufunkhidwa; ndi nyumba zao zabwinja; adzamangadi nyumba, koma sadzagonamo; adzanka minda yampesa koma sadzamwa vinyo wace.

14. Tsiku lalikuru la Yehova liri pafupi, liri pafupi lifulumira kudza, mau a tsiku la Yehova; munthu wamphamvu adzalirapo mowawa mtima.

15. Tsikulo ndi tsiku la mkwiyo, tsiku la msauko ndi lopsinja tsiku la bwinja, ndi cipasuko, tsiku la mdima ndi la cisisira, tsiku la mitambo ndi lakuda bii;

Zefaniya 1