1. Koma ku Yeriko anatseka pazipata, natsekedwa cifukwa ca ana a Israyeli, panalibe woturuka, panalibenso wolowa.
2. Ndipo Yehova ananena kwa Yoswa, Taona, ndapereka m'dzanja lako Yeriko ndi mfumu yace, ndi ngwazi zace.
3. Ndipo muzizungulira mudzi Inu nonse ankhondo, kuuzungulira mudzi kamodzi. Muzitero masiku asanu ndi limodzi.
4. Ndipo ansembe asanu ndi awiri azinyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga: za nkhosa zamphongo, natsogolere nazo likasa; koma tsiku lacisanu ndi ciwiri muzizungulira mudziwo kasanu ndi kawirio ndi ansembe aziliza mphalasazo.
5. Ndipo kudzakhala kuti akaliza cilizire ndi nyanga ya nkhosa yamphongo, nimumva kulira kwa mphalasa, anthu onse apfuule mpfuu yaikuru; ndipo linga la mudziwo lidzagwa pomwepo, ndi anthu adzakwera ndi kulowamo yense kumaso kwace.