Yoswa 21:1-2 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo akuru a nyumba za atate a Alevi anayandikira kwa Eleazare wansembe, ndi kwa Yoswa mwana wa Nuni, ndi kwa akuru a nyumba za atate a mapfuko a ana a Israyeli;

2. nanena nao ku Silo m'dziko la Kanani, ndi kuti Yehova analamulira mwa dzanja la Mose kuti atipatse midzi yokhalamo ife, ndi mabusa a zoweta zathu.

Yoswa 21