6. Ndipo azikhala m'mudzimo mpaka adzaima pamaso pa msonkhano anene mlandu wace, mpaka atafa mkulu wansembe wa m'masiku omwewo; pamenepo wakupha mnzace azibwerera ndi kufika kumudzi kwace, ndi nyumba yace, kumudzi kumene adathawako.
7. Ndipo anapatula Kedesi m'Galileya ku mapiri a Nafitali, ndi Sekemu ku mapiri a Efraimu, ndi mudzi wa Ariba ndiwo Hebroni ku mapiri a Yuda.
8. Ndipo tsidya lija la Yordano kum'mawa kwa Yeriko, anaika Bezeri m'cipululu, kucidikha, wa pfuko la Rubeni, ndi Ramoti m'Gileadi wa ofuko la Gadi, ndi Golani m'Basana wa pfuko la Manase.