15. Ngati mukonda Ine, sungani malamulo anga.
16. Ndipo Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe yina, kuti akhale ndi inu ku nthawi yonse,
17. ndiye Mzimu wa coonadi; amene dziko lapansi silingathe kumlandira, pakuti silimuona iye, kapena kumzindikira iye. Inu mumzindikira iye; cifukwa akhala ndi inu nadzakhala mwa inu.
18. Sindidza-kusiyani inu mukhale ana amasiye; ndidza kwa inu.
19. Katsala kanthawi, ndipo dziko lapansi silindionanso Ine; koma inu mundiona; popeza Ine ndiri ndi moyo inunso mudzakhala ndi moyo.
20. Tsiku lo mwelo mudzazindikira kuti ndiri Ine mwa Atate wanga, ndi inu mwa Ine, ndi Ine mwa inu.