Yesaya 65:1-2 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Iwo amene sanafunsa za Ine andifunafuna; ndi iwo amene sanandipwaira andipeza; ndinati, Taonani Ine, taonani Ine, kwa mtundu umene sunachula dzina langa.

2. Ndatambasulira manja anga tsiku lonse kwa anthu opanduka, amene ayenda m'njira mosati mwabwino, kutsata maganizo ao ao;

Yesaya 65