Yesaya 56:1-2 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Atero Yehova, Sungani inu ciweruziro, ndi kucita cilungamo; pakuti cipulumutso canga ciri pafupi kudza, ndi cilungamo canga ciri pafupi kuti cib zumbulutsidwe,

2. Wodala munthu amene acita ici, ndi mwana wa munthu amene agwira zolimba ici, amene asunga sabata osaliipitsa, nasunga dzanja lace osacita nalo coipa ciri conse.

Yesaya 56