Yesaya 44:6-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Atero Yehova, Mfumu ya Israyeli ndi Mombolo wace, Yehova wa makamu, Ine ndiri woyamba ndi womariza, ndi popanda Ine palibenso Mulungu.

7. Ndipo ndani adzaitana monga Ine, ndi kulalikira ici ndi kundilongosolera ici, cikhazikitsire Ine anthu akale? milunguyo iwadziwitse zomwe zirinkudza, ndi za m'tsogolo.

8. Musaope inu, musakhale ndi mantha; kodi ndinanena kwa iwe zakale, ndi kuzionetsa zimenezo, ndipo inu ndinu mboni zanga. Kodi popanda Ine aliponso Mulungu? Iai, palibe thanthwe; sindidziwa liri lonse.

9. Omwe apanga fano losema onsewo asokonezeka; ndipo zokondweretsa zao sadzapindula nazo kanthu; ndipo mboni zao siziona, kapena kudziwa; kuti akhale ndi manyazi.

10. Ndani wapanga mulungu, kapena kusungunula fano losema losapindula kanthu?

11. Taonani anzace onse adzakhala ndi manyazi, ndi amisiri ace ndi anthu; asonkhane onse pamodzi, aimirire; adzaopa, iwo onse adzakhala ndi manyazi.

12. Wacipala acita zace ndi nsompho, nagwira nchito ndi makala, nafanizira fanolo ndi nyundo, nagwira nchito yace ndi mkono wace wamphamvu; inde, ali ndi njala, ndipo mphamvu zace zilephera; iye samwa madzi, nalefuka.

Yesaya 44