Yesaya 42:9-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Taona, zinthu zakale zaoneka, ndipo zatsopano Ine ndizichula; zisanabuke ndidzakumvetsani.

10. Yimbirani Yehova nyimbo yatsopano, ndi matamando ace kucokera ku malekezero a dziko lapansi; inu amene mutsikira kunyanja, ndi zonse ziri m'menemo, zisumbu ndi okhala mommo.

11. Cipululu ndi midzi yace ikweze mau ao, midzi imene Kedara akhalamo; okhala m'Sela ayimbe, akuwe kucokera pamwamba pa mapiri.

12. Apereke ulemerero kwa Yehova, anene matamando ace m'zisumbu.

13. Yehova adzaturuka ngati munthu wamphamvu; adzautsa nsanje ngati munthu wa nkhondo; Iye adzapfuula, inde adzakuwa zolimba; adzacita zamphamvu pa adani ace.

14. Ndakhala nthawi yambiri wosalankhula; ndakhala cete ndi kudzithungata ndekha; tsopano ndidzapfuula ngati mkazi wobala; ndidzapuma modukizadukiza ndi wefuwefu pamodzi.

15. Ndidzapasula mapiri ndi zitunda, ndi kuumitsa zitsamba zao zonse; ndi kusandutsa nyanja zisumbu, ndi kuumitsa matamanda.

16. Ndipo ndidzayendetsa akhungu m'khwalala, limene iwo salidziwa; m'njira zimene iwo sazidziwa ndidzawatsogolera; ndidzawalitsa mdima m'tsogolo mwao, ndi kulungamitsa malo okhota. Zinthu Izi ine ndidzacita, ndipo sindidzawasiya.

Yesaya 42