1. Ha, dziko lakukupuza mapiko, liri tsidya lija la nyanja za Etiopia;
2. limene litumiza mithenga panyanja m'ngalawa zatnabungwa zoyenda m'madzi, ndi kuti, Mukani, inu mithenga yoyenda msanga msanga ku mtundu wa anthu atari ndi osalala, kwa mtundu woopsya cikhalire cao, mtundu umene uyesa dziko ndi kupondereza pansi, umene dziko lace nyanja ziligawa!
3. Inunonseakukhala m'dziko lapansi, ndi inu akukhazikika pa dziko lapansi, potukulidwa cizindikiro pamwamba pa mapiri, mudzaona, ndi polizidwa lipenga mudzamva.