Yesaya 17:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Katundu wa Damasiko. Taonani, Damasiko wacotsedwa usakhalenso mudzi, ndimo udzangokhala muunda wopasudwa.

2. Midzi ya Aroeri yasiyidwa; idzakhala ya zoweta zogona pansi, opanda woziopsya.

3. Ku Efraimu sikudzakhalanso linga, ngakhale ufumu ku Damasiko, ngakhale otsala kwa Aramu; iwo adzakhala ngati ulemerero wa ana a Israyeli, ati Yehova wamakamu.

4. Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti ulemerero wa Yakobo udzakhala wopyapyala, ndi kunenepa kwa thupi lace kudzaonda.

Yesaya 17